6. cingwe casiliva cisanaduke, ngakhale mbale yagolidi isanasweke, ngakhale mtsuko usanaphwanyike kukasupe, ngakhale njinga yotungira madzi isanatyoke kucitsime;
7. pfumbi ndi kubwera pansi pomwe linali kale, mzimu ndi kubwera kwa Mulungu amene anaupereka.
8. Cabe zacabetu, ati Mlalikiyo; zonse ndi cabe.
9. Ndiponso pokhala wanzeru Mlalikiyo anaphunzitsabe anthu nzeru; inde, anachera makutu nafunafuna nalongosolamiyambiyambiri.
10. Mlalikiyo anasanthula akapeze mau okondweretsa, ndi zolemba zoongoka ngakhale mau oona.
11. Mau a anzeru akunga zisonga, omwe akundika mau amene mbusa mmodzi awapatsa mau ao akunga misomali yokhomedwa zolimba.
12. Pamodzi ndi izi, mwananga, tacenjezedwa; pakuti saleka kulemba mabuku ambiri; ndipo kuphunzira kwambiri kutopetsa thupi.
13. Mau atha; zonse zamveka zatha; opa Mulungu, musunge malamulo ace; pakuti coyenera anthu onse ndi ici.
14. Pakuti Mulungu adzanena mlandu wa zocita zonse, ndi zobisika zonse, ngakhale zabwino ngakhale zoipa.