1. Ukumbukirenso Mlengi wako masiku a unyamata wako, asanadze masiku oipa, ngakhale zisanayandikire zakazo zakuti udzati, Sindikondwera nazo;
2. ngakhale lisanade dzuwa, ndi kuunika, ndi mwezi, ndi nyenyezi, mitambo ndi kubweranso italeka mvula;
3. tsikulo omwe asunga nyumba adzanthunthumira, amuna olimba nadzawerama, akupera nadzaleka poperewera, omwe ayang'ana pamazenera nadzadetsedwa;
4. pa khomo lakunja padzatsekeka; potsika mau akupera, wina nanyamuka polira mbalame, ndipo akazi onse akuyimba sadzamveka bwino;
5. inde, adzaopa za pamwamba, panjira padzakhala zoopsya; mciu nudzaphuka, dzombe ndi kukoka miyendo, zilakolako ndi kutha; pakuti munthu apita kwao kwamuyaya, akulira maliro nayendayenda panja;