4. Ngati mkuru akukwiyira, usasiye malo ako; cifukwa cifatso cipembedza utacimwa kwambiri.
5. Pali coipa ndaciona pansi pano, ngati kulakwa koyambira ndi mkuru;
6. utsiru ukhazikika pamwamba penipeni, ndipo olemera angokhala mwamanyazi.
7. Ndaona akapolo atakwera pa akavalo, ndi mafumu, alikuyenda pansi ngati akapolo.
8. Wokumba mbuna adzagwamo; ndipo woboola mpanda njoka idzamluma.
9. Wosendeza miyala adzaphwetekedwa nayo; wowaza nkhuni nadzitema.
10. Citsulo cikakhala cosathwa, ndipo ukaleka kunola, uzipambana kulimbikira; koma nzeru ipindulira pocenjeza.
11. Njoka ikaluma isanalodzedwe, watsenga saona mphotho.
12. Mau a m'kamwa mwa munthu wanzeru nga cisomo; koma milomo ya citsiru idzacimeza.