Mlaliki 10:1-3 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Nchenche zakufa zinunkhitsa moipa nizioletsa mafuta onunkhira a sing'anga; comweco kupusa kwapang'ono kuipitsa iye amene achuka cifukwa ca nzeru ndi ulemu.

2. Wanzeru, mtima wace uli ku dzanja lace lamanja; koma citsiru, mtima wace kulamanzere.

3. Inde, poyendanso citsiru panjira, nzeru yace imthera ndipo angoti kwa onse kuti, Ndine citsiru.

Mlaliki 10