1. Nchenche zakufa zinunkhitsa moipa nizioletsa mafuta onunkhira a sing'anga; comweco kupusa kwapang'ono kuipitsa iye amene achuka cifukwa ca nzeru ndi ulemu.
2. Wanzeru, mtima wace uli ku dzanja lace lamanja; koma citsiru, mtima wace kulamanzere.
3. Inde, poyendanso citsiru panjira, nzeru yace imthera ndipo angoti kwa onse kuti, Ndine citsiru.
4. Ngati mkuru akukwiyira, usasiye malo ako; cifukwa cifatso cipembedza utacimwa kwambiri.
5. Pali coipa ndaciona pansi pano, ngati kulakwa koyambira ndi mkuru;
6. utsiru ukhazikika pamwamba penipeni, ndipo olemera angokhala mwamanyazi.
7. Ndaona akapolo atakwera pa akavalo, ndi mafumu, alikuyenda pansi ngati akapolo.
8. Wokumba mbuna adzagwamo; ndipo woboola mpanda njoka idzamluma.
9. Wosendeza miyala adzaphwetekedwa nayo; wowaza nkhuni nadzitema.
10. Citsulo cikakhala cosathwa, ndipo ukaleka kunola, uzipambana kulimbikira; koma nzeru ipindulira pocenjeza.