Miyambi 9:1-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Nzeru yamanga nyumba yace,Yasema zoimiritsa zace zisanu ndi ziwiri;

2. Yaphera nyama yace, nisanganiza vinyo wace,Nilongosolanso pa gome lace.

3. Yatuma anamwali ace, iitanaPa misanje ya m'mudzi.

4. Wacibwana yense apambukire kuno;Iti kwa yense wosowa nzeru,

5. Tiyeni, idyani cakudya canga;Nimumwe vinyo wanga ndamsanganiza.

6. Lekani, acibwana inu, nimukhale ndi moyo;Nimuyende m'njira ya nzeru.

7. Woweruza munthu wonyoza adzicititsa yekha manyazi;Yemwe adzudzula wocimwa angodetsa mbiri yace yace.

8. Usadzudzule wonyoza kuti angakude;Dzudzula wanzeru adzakukonda.

9. Ukacenjeza wanzeru adzakulitsa nzeru yace;Ukaphunzitsa wolungama adzaonjezera kuphunzira,

10. Ciyambi ca nzeru ndico kuopa Yehova;Kudziwa Woyerayo ndiko luntha;

11. Pakuti mwa ine masiku ako adzacuruka,Zaka za moyo wako zidzaonjezedwa.

Miyambi 9