Miyambi 8:24-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

24. Pamene panalibe zozama ndinabadwa ine,Pamene panalibe akasupe odzala madzi.

25. Mapiri asanakhazikike,Zitunda zisanapangidwe, ndinabadwa;

26. Asanalenge dziko, ndi thengo,Ngakhale ciyambi ca pfumbi la dziko.

27. Pamene anakhazika mlengalenga ndinali pompo;Pamene analemba pazozama kwete kwete;

28. Polimbitsa Iye thambo la kumwamba,Pokula akasupe a zozama.

29. Poikira nyanja malire ace,Kuti madzi asapitirire pa lamulo lace;Polemba maziko a dziko,

30. Ndinali pa mbali pace ngati mmisiri;Ndinamsekeretsa tsiku ndi tsiku,Ndi kukondwera pamaso pace nthawi zonse;

Miyambi 8