Miyambi 8:2-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Iima pamwamba pa mtunda,Pa mphambano za makwalala;

3. Pambali pa cipata polowera m'mudzi,Polowa anthu pa makomo ipfuula:

4. Ndinu ndikuitanani, amuna,Mau anga ndilankhula kwa ana a anthu.

5. Acibwana inu, cenjerani,Opusa inu, khalani ndi mtima wozindikira;

6. Imvani, pakuti ndikanena zoposa,Ndi zolungama potsegula pakamwa panga,

7. Pakuti m'kamwa mwanga mudzalankhula ntheradi,Zoipa zinyansa milomo yanga.

8. Mau onse a m'kamwa mwanga alungama;Mwa iwo mulibe zokhota ndi zopotoka.

9. Onsewo amveka ndi iye amene azindikira;Alungama kwa akupeza nzeru.

10. Landirani mwambo wanga, si siliva ai;Ndi nzeru kopambana ndi golidi wosankhika.

11. Pakuti nzeru iposa ngale,Ndi zonse tizifunitsa sizilingana nayo,

12. Ine Nzeru ndikhala m'kucenjera, ngati m'nyumba yanga;Ndimapeza kudziwa ndi zolingalira.

Miyambi 8