Miyambi 8:12-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Ine Nzeru ndikhala m'kucenjera, ngati m'nyumba yanga;Ndimapeza kudziwa ndi zolingalira.

13. Kuopa Yehova ndiko kuda zoipa;Kunyada, ndi kudzikuza, ndi njira yoipa, ndi m'kamwa mokhota, ndizida.

14. Ndine mwini uphungu ndi kudziwitsa;Ndine luntha; ndiri ndi mphamvu.

15. Mwa ine mafumu alamulira;Akazembe naweruza molungama.

16. Mwa ine akalonga ayang'anira,Ndi akuru, ngakhale oweruza onse a m'dziko,

17. Akundikonda ndiwakonda;Akundifunafuna adzandipeza.

18. Katundu ndi ulemu ziri ndi ine,Cuma cosatha ndi cilungamo.

Miyambi 8