Miyambi 8:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Kodi nzeru siitana,Luntha ndi kukweza mau ace?

2. Iima pamwamba pa mtunda,Pa mphambano za makwalala;

3. Pambali pa cipata polowera m'mudzi,Polowa anthu pa makomo ipfuula:

4. Ndinu ndikuitanani, amuna,Mau anga ndilankhula kwa ana a anthu.

5. Acibwana inu, cenjerani,Opusa inu, khalani ndi mtima wozindikira;

6. Imvani, pakuti ndikanena zoposa,Ndi zolungama potsegula pakamwa panga,

Miyambi 8