Miyambi 6:5-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Dzipulumutse wekha ngati mphoyo ku dzanja la msaki,Ndi mbalame ku dzanja la msodzi.

6. Pita kunyerere, wolesi iwe,Penya njira zao nucenjere;

7. Ziribe mfumu,Ngakhale kapitao, ngakhale mkuru;

8. Koma zitengeratu zakudya zao m'malimwe;Nizituta dzinthu zao m'masika.

9. Udzagona mpaka liti, wolesi iwe?Udzauka ku tulo tako liti?

10. Tulo ta pang'ono, kuodzera pang'ono,Kungomanga manja pang'ono, ndi kugona;

11. Ndipo umphawi wako udzafika ngati mbala,Ndi kusauka kwako ngati munthu wacikopa.

Miyambi 6