Miyambi 6:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Mwananga, ngati waperekera mnzako cikole,Ngati wapangana kulipirira mlendo,

2. Wakodwa ndi mau a m'kamwa mwako,Wagwidwa ndi mau a m'kamwa mwako.

3. Cita ici tsono; mwananga, nudzipulumutse;Popeza walowa m'dzanja la mnzako,Pita nudzicepetse, numdandaulire mnzako,

4. Usaone tulo m'maso mwako,Ngakhale kuodzera zikope zako.

Miyambi 6