Miyambi 31:22-31 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

22. Adzipangira zimbwi zamaangamaanga;Nabvala bafuta ndi guta woti biriwiri.

23. Mwamuna wace adziwika kubwalo,Pokhala pakati pa akuru a dziko.

24. Asoka maraya abafuta, nawagulitsa;Napereka mipango kwa wogulitsa malonda.

25. Abvala mphamvu ndi ulemu;Nangoseka nthawi ya m'tsogolo.

26. Atsegula pakamwa pace ndi nzeru,Ndipo cilangizo ca cifundo ciri pa lilime lace.

27. Ayang'anira mayendedwe a banja lace,Sadya zakudya za ulesi.

28. Anace adzanyamuka, nadzamucha wodala;Mwamuna wace namtama, nati,

29. Ana akazi ambiri anacita mwangwiro,Koma iwe uposa onsewo.

30. Kukongola kungonyenga, maonekedwe okoma ndi cabe;Koma mkazi woopa Yehova adzatamandidwa.

31. Mumpatse zipatso za manja ace; Ndi nchito zace zimtame kubwalo.

Miyambi 31