Miyambi 31:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Mau a Lemueli mfumu, uthenga umene amace anamphunzitsa.

2. Ciani mwananga, Ciani mwana wa mimba yanga?Ciani mwana wa zowinda zanga?

3. Musapereke mphamvu yako kwa akazi,Ngakhale kuyenda m'njira yoononga mafumu.

4. Mafumu, Lemueli, mafumu sayenera kumwa vinyo;Akalonga sayenera kunena, Cakumwa caukali ciri kuti?

Miyambi 31