Miyambi 29:7-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Wolungama asamalira mlandu wa osauka;Koma woipa alibe nzeru yakuudziwa.

8. Anthu onyoza atentha mudzi;Koma anzeru alezetsa mkwiyo.

9. Munthu wanzeru akatsutsana ndi munthu wopusa,Ngakhale akwiya, ngakhale aseka, palibe mtendere.

10. Anthu ankhanza ada wangwiro;Koma oongoka mtima asamalira moyowace.

11. Citsiru cibvumbulutsa mkwiyo wace wonse;Koma wanzeru auletsa nautontholetsa.

12. Mkuru akamvera cinyengo,Atumuki ace onse ali oipa,

13. Waumphawi ndi wotsendereza akumana;Yehova apenyetsa maso a onse awiriwo.

14. Mfumu yolamulira osauka mwantheradi,Mpando wace udzakhazikika kufikira nthawi zonse.

Miyambi 29