Miyambi 28:11-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Wolemera adziyesa wanzeru;Koma wosauka wozindikira aululitsa zace.

12. Posekera olungama pali ulemerero wambiri;Koma pouka oipa anthu amabisala.

13. Wobisa macimo ace sadzaona mwai;Koma wakuwabvomereza, nawasiya adzacitidwa cifundo.

14. Wodala munthu wakuopakosalekeza;Koma woumitsa mtima wace adzagwa m'zoipa.

15. Monga mkango wobangula ndi cirombo coyendayenda,Momwemo mfumu yoipa ya anthu osauka.

16. Kalonga wosowa nzeru apambana kusautsa;Koma yemwe ada cisiriro adzatanimphitsa moyo wace.

17. Woparamula mlandu wakupha munthu adzathawira kudzenje;Asamuletse.

18. Woyenda mwangwiro adzapulumuka;Koma wokhota m'mayendedwe ace adzagwa posacedwa.

Miyambi 28