Miyambi 28:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Woipaathawapalibewomthamangitsa;Koma olungama alimba mtima ngati mkango.

2. Pocimwa dziko akalonga ace acuruka;Koma anthu ozindikira ndi odziwa alikhazikikitsa nthawi yaikuru.

3. Munthu waumphawi wotsendereza osaukaAkunga mvula yamadzi yokokolola dzinthu.

4. Omwe asiya cilamulo atama oipa;Koma omwe asunga cilamulo akangana nao.

5. Oipa samvetsetsa ciweruzo;Koma omwe afuna Yehova amvetsetsa zonse.

Miyambi 28