Miyambi 27:11-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Mwananga, khala wanzeru, nukondweretse mtima wanga;Kuti ndimuyankhe yemwe anditonza.

12. Wocenjera aona zoipa, nabisala;Koma acibwana angopitirira, nalipitsidwa.

13. Tenga maraya a woperekera mlendo cikole;Woperekera mkazi waciwerewere cikole umgwire mwini.

14. Yemwe adalitsa mnzace ndi mau akuru pouka mamawa,Anthu adzaciyesa cimeneco temberero.

15. Kudonthadontha tsiku lamvula,Ndi mkazi wolongolola ali amodzimodzi.

Miyambi 27