Miyambi 26:18-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Monga woyaruka woponya nsakali,Mibvi, ndi imfa,

19. Momwemo wonyenga mnzace ndi kuti, Ndi kusewera kumeneku.

20. Posowa nkhuni moto ungozima;Ndi popanda kazitape makangano angoleka.

21. Monga makala ozizira pa makala akunyeka, ndi nkhuni pamoto;Momwemo munthu wamakangano autsa ndeu.

Miyambi 26