25. Monga madzi ozizira kwa munthu wotopa,Momwemo mau abwino akucokera ku dziko lakutari.
26. Monga kasupe wopondedwa, ndi citsime cobvonongeka,Momwemo wolungama ngati akonjera woipa.
27. Kudya uci wambiri sikuli kwabwino;Comweco kufunafuna ulemu wako wako sikuli ulemu.
28. Wosalamulira mtima waceAkunga mudzi wopasuka wopanda linga,