20. Monga wobvula maraya tsiku lamphepo,Ngakhale kuthira vinyo wosasa m'soda,Momwemo woyimbira nyimbo munthu wacisoni.
21. Mdani wako akamva njala umdyetse,Akamva ludzu ummwetse madzi,
22. Pakuti udzaunjika makala amoto pamtu pace;Ndipo Yehova adzakupatsa mphotho,
23. Mphepo ya kumpoto ifikitsa mvula;Comweco lilime losinjirira likwiyitsa nkhope.
24. Kukhala pa ngondya ya tsindwi kufunikaKuposa kukhala m'nyumba ndi mkazi wolongolola.
25. Monga madzi ozizira kwa munthu wotopa,Momwemo mau abwino akucokera ku dziko lakutari.