Miyambi 25:2-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Kubisa kanthu ndi ulemerero wa Mulungu;Koma ulemerero wa mafumu ndi kusanthula kanthu.

3. Pamlengalenga patarika, ndi padziko pakuya,Koma mitima ya mafumu singasanthulike.

4. Cotsera siliva mphala yace,Mmisiri wa ng'anjo aturutsamo mbale;

5. Cotsera woipa pamaso pa mfumu,Mpando wace udzakhazikika m'cilungamo.

6. Usadzitame pamaso pa mfumu,Ngakhale kuima m'malo mwa akuru;

Miyambi 25