1. Iyinso ndiyo miyambo ya SolomoImene anthu a Hezekiya mfumu ya Yuda anailemba.
2. Kubisa kanthu ndi ulemerero wa Mulungu;Koma ulemerero wa mafumu ndi kusanthula kanthu.
3. Pamlengalenga patarika, ndi padziko pakuya,Koma mitima ya mafumu singasanthulike.