Miyambi 22:9-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Mwini diso lamataya adzadala;Pakuti apatsa osauka zakudya zace.

10. Ukainga wonyoza, makangano adzaturuka;Makani ndi manyazi adzalekeka.

11. Wokonda kuyera mtima,Mfumu idzakhala bwenzi lace cifukwa ca cisomo ca milomo yace.

12. Maso a Yehova acinjiriza wodziwa;Koma agwetsa mau a munthu wa ziwembu.

13. Waulesi ati, Pali mkango panjapo,Ndidzaphedwa pamakwalalapo.

14. M'kamwa mwa mkazi waciwerewere muli dzenje lakuya;Yemwe Yehova amkwiyira adzagwamo.

15. Utsiru umangidwa mumtima mwa mwana;Koma ntyole yomlangira idzauingitsira kutari.

16. Wotsendereza waumphawi kuti acurukitse cuma cace,Ndi wopatsa wolemera kanthu, angosauka.

17. Chera makutu ako, numvere mau a anzeru,Nulozetse mtima wako kukadziwa zanga.

Miyambi 22