Miyambi 20:27-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

27. Mzimu wa munthu ndiwo nyali ya Yehova;Usanthula m'kati monse mwa mimba.

28. Cifundo ndi ntheradi zisunga mfumu;Cifundo cicirikiza mpando wace.

29. Ulemerero wa anyamata ndiwo mphamvu yao;Kukongola kwa nkhalamba ndi

30. Mikwingwirima yopweteka icotsa zoipa;Ndi mikwapulo ilowa m'kati mwa mimba.

Miyambi 20