25. Kunena mwansontho, ici ncopatulika, kuli msampha kwa munthu,Ndi kusinkhasinkha pambuyo pace atawinda.
26. Mfumu yanzeru ipeta amphulupulu,Niyendetsapo njinga ya gareta.
27. Mzimu wa munthu ndiwo nyali ya Yehova;Usanthula m'kati monse mwa mimba.
28. Cifundo ndi ntheradi zisunga mfumu;Cifundo cicirikiza mpando wace.