Miyambi 20:20-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. Wotemberera atate wace ndi, amace,Nyali yace idzazima mu mdima woti bi.

21. Colowa cingalandiridwe msanga msanga poyamba pace;Koma citsiriziro cace sicidzadala.

22. Usanene, Ndidzabwezera zoipa;Yembekeza Yehova, adzakupulumutsa.

23. Miyeso yosiyana inyansa Yehova,Ndi mulingo wonyenga suli wabwino.

24. Yehova alongosola mayendedwe a mwamuna;Munthu tsono angazindikire bwanji njira yace?

25. Kunena mwansontho, ici ncopatulika, kuli msampha kwa munthu,Ndi kusinkhasinkha pambuyo pace atawinda.

26. Mfumu yanzeru ipeta amphulupulu,Niyendetsapo njinga ya gareta.

Miyambi 20