Miyambi 20:18-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Uphungu utsimikiza zolingalira,Ponya nkhondo utapanga upo.

19. Kazitape woyendayenda awanditsa zinsinsi;Usadudukire woyasama milomo yace.

20. Wotemberera atate wace ndi, amace,Nyali yace idzazima mu mdima woti bi.

21. Colowa cingalandiridwe msanga msanga poyamba pace;Koma citsiriziro cace sicidzadala.

22. Usanene, Ndidzabwezera zoipa;Yembekeza Yehova, adzakupulumutsa.

23. Miyeso yosiyana inyansa Yehova,Ndi mulingo wonyenga suli wabwino.

24. Yehova alongosola mayendedwe a mwamuna;Munthu tsono angazindikire bwanji njira yace?

Miyambi 20