13. Usakonde tulo ungasauke;Phenyula maso, udzakhuta zakudya.
14. Wogula ati, Cacabe cimeneco.Koma atacoka adzitama.
15. Alipo golidi ndi ngale zambiri;Koma milomo yodziwa ndiyo cokometsera ca mtengo wapatari.
16. Tenga maraya a woperekera mlendo cikole;Woperekera mkazi wacilendo cikole umgwire mwini.
17. Zakudya za cinyengo zikondweretsa munthu;Koma pambuyo pace m'kamwa mwace mudzadzala tinsangalabwi.