Miyambi 19:6-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Ambiri adzapembedza waufulu;Ndipo yense ndi bwenzi la munthu wopatsa.

7. Abale onse a wosauka amuda;Nanga mabwenzi ace kodi satanimphirana naye?Awatsata ndi mau, koma kuli zi.

8. Wolandira nzeru akonda moyo wace;Wosunga luntha adzapeza zabwino.

9. Mboni yonama sidzapulumuka cilango;Wolankhula mabodza adzaonongeka.

10. Wopusa sayenera kukhala ndi zinthu zolongosoka;Nanga kapolo ayenera kulamulira akalonga kodi?

11. Kulingalira kwa munthu kucedwetsa mkwiyo;Ulemerero wace uli wakuti akhululukire colakwa.

12. Mkwiyo wa mfumu ukunga kubangula kwa mkango;Koma kukoma mtima kwace kunga mame pamsipu.

Miyambi 19