Miyambi 19:26-29 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

26. Wolanda za atate, ndi wopitikitsa amai,Ndiye mwana wocititsa manyazi ndi wogwetsa nkhope.

27. Ukangofuna, mwananga, kusocera kusiya mau akudziwitsa,Leka kumva mwambo.

28. Mboni yopanda pace inyoza ciweruzo;M'kamwa mwa amphulupulu mumeza zoipa,

29. Akonzera onyoza ciweruzo,Ndi mikwingwirima pamsana pa opusa.

Miyambi 19