Miyambi 19:19-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Munthu waukali alipire mwini;Pakuti ukampulumutsa udzateronso.

20. Tamvera uphungu, nulandire mwambo,Kuti ukhale wanzeru pa cimariziro cako,

21. Muli zolingalira zambiri m'mtima mwa munthu;Koma uphungu wa Yehova ndiwo udzaimika.

22. Cotikondetsa munthu ndico kukoma mtima kwace;Ndipo wosauka apambana munthu wonama.

23. Kuopa Yehova kupatsa moyo;Wokhala nako adzakhala wokhuta;Zoipa sizidzamgwera.

24. Wolesi alonga dzanja lace m'mbale,Osalibwezanso kukamwa kwace.

25. Menya wonyoza, ndipo acibwana adzaceniera;Nudzudzule wozindikira adzazindikira nzeru.

26. Wolanda za atate, ndi wopitikitsa amai,Ndiye mwana wocititsa manyazi ndi wogwetsa nkhope.

27. Ukangofuna, mwananga, kusocera kusiya mau akudziwitsa,Leka kumva mwambo.

Miyambi 19