Miyambi 18:9-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Wogwira nchito mwaulesiNdiye mbale wace wa wosakaza.

10. Dzina la Yehova ndilo linga lolimba;Wolungama athamangiramo napulumuka.

11. Cuma ca wolemera ndico mudzi wace wolimba;Alingalira kuti ndico khoma lalitari.

12. Mtima wa munthu unyada asanaonongeke;Koma cifatso citsogolera ulemu.

13. Wobwezera mau asanamvetse apusa,Nadzicititsa manyazi.

Miyambi 18