Miyambi 18:14-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Mtima wa munthu umlimbitsa alikudwala;Koma ndani angatukule mtima wosweka?

15. Mtima wa wozindikira umaphunzira;Khutu la anzeru lifunitsa kudziwa.

16. Mtulo wa munthu umtsegulira njira,Numfikitsa pamaso pa akuru.

17. Woyamba kudzinenera ayang'anika wolungama;Koma mnzace afika namuululitsa zace zonse.

18. Ula uletsa makangano,Nulekanitsa amphamvu.

19. Kupembedza mbale utamcimwira nkobvuta,Kulanda mudzi wolimba nkosabvuta;Makangano akunga mipiringidzo ya linga.

20. Mimba ya munthu idzakhuta zipatso za m'kamwa mwace;Iye nadzakhuta phindu la milomo yace.

21. Lilime liri ndi mphamvu pa imfa ndi moyo;Wolikonda adzadya zipatso zace.

Miyambi 18