Miyambi 16:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Malongosoledwe a mtima nga munthu;Koma mayankhidwe a lilime acokera kwa Yehova.

2. Njira zonse za munthu ziyera pamaso pace;Koma Yehova ayesa mizimu.

3. Pereka zocita zako kwa Yehova,Ndipo zolingalira zako zidzakhazikika.

4. Zonse Yehova anazipangaziri ndi zifukwa zao;Ngakhale amphulupulu kuti aone tsiku loipa,

5. Yense wonyada mtima anyansa Yehova;Zoonadi sadzapulumuka cilango.

Miyambi 16