Miyambi 15:29-33 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

29. Yehova atarikira oipa;Koma pemphero la olungama alimvera.

30. Kuunika kwa maso kukondweretsa mtima;Ndipo pomveka zabwino mafupa amatenga uwisi.

31. Khutu lomvera cidzudzulo ca moyoLidzakhalabe mwa anzeru.

32. Wokana mwambo apeputsa moyo wace;Koma wosamalira cidzudzulo amatenga nzeru.

33. Kuopa Yehova ndiko mwambo wanzeru;Ndipo cifatso citsogolera ulemu.

Miyambi 15