Miyambi 15:27-31 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

27. Wopindula monyenga abvuta nyumba yace;Koma wakuda mitulo adzakhala ndi moyo.

28. Mtima wa wolungama uganizira za mayankhidwe;Koma m'kamwa mwa ocimwa mutsanulira zoipa.

29. Yehova atarikira oipa;Koma pemphero la olungama alimvera.

30. Kuunika kwa maso kukondweretsa mtima;Ndipo pomveka zabwino mafupa amatenga uwisi.

31. Khutu lomvera cidzudzulo ca moyoLidzakhalabe mwa anzeru.

Miyambi 15