Miyambi 15:21-33 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

21. Wosowa nzeru akondwera ndi utsiru;Koma munthu wozindikira aongola mayendedwe ace.

22. Zolingalira zizimidwa popanda upoKoma pocuruka aphungu zikhazikika.

23. Munthu akondwera ndi mayankhidwe a m'kamwa mwace;Ndi mau a pa nthawi yace kodi sali abwino?

24. Anzeru ayesa njira yamoyo yokwerakwera,Kuti apambuke kusiya kunsi kwa manda.

25. Yehova adzapasula nyumba ya wonyada;Koma adzalembera mkazi wamasiye malire ace,

26. Ziwembu zoipa zinyansa Yehova;Koma oyera mtima alankhula mau okondweretsa.

27. Wopindula monyenga abvuta nyumba yace;Koma wakuda mitulo adzakhala ndi moyo.

28. Mtima wa wolungama uganizira za mayankhidwe;Koma m'kamwa mwa ocimwa mutsanulira zoipa.

29. Yehova atarikira oipa;Koma pemphero la olungama alimvera.

30. Kuunika kwa maso kukondweretsa mtima;Ndipo pomveka zabwino mafupa amatenga uwisi.

31. Khutu lomvera cidzudzulo ca moyoLidzakhalabe mwa anzeru.

32. Wokana mwambo apeputsa moyo wace;Koma wosamalira cidzudzulo amatenga nzeru.

33. Kuopa Yehova ndiko mwambo wanzeru;Ndipo cifatso citsogolera ulemu.

Miyambi 15