Miyambi 15:13-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Mtima wokondwa usekeretsa nkhope;Koma moyo umasweka ndi zowawa za m'mtima.

14. Mtima wa wozindikira ufunitsa kudziwa;Koma m'kamwa mwa opusa mudya utsiru.

15. Masiku onse a wosauka ali oipa;Koma wokondwera mtima ali ndi phwando losatha.

16. Zapang'ono, ulikuopa Yehova,Zipambana ndi katundu wambiri pokhala phokoso,

17. Kudya masamba, pali cikondano,Kuposa ng'ombe yonenepa pali udani.

18. Munthu wozaza aputa makani;Koma wosakwiya msanga atonthoza makangano.

19. Mayendedwe a wolesi akunga Hnga laminga,Koma njira ya oongoka mtima iundidwa ngati mseu.

20. Mwana wanzeru akondweretsa atate wace;Koma munthu wopusa apeputsa amace.

21. Wosowa nzeru akondwera ndi utsiru;Koma munthu wozindikira aongola mayendedwe ace.

Miyambi 15