24. Korona wa anzeru ndi cuma cao;Utsiru wa opusa ndiwo utsiru.
25. Mboni yoona imalanditsa miyoyo;Koma wolankhula zonama angonyenga.
26. Wakuopa Yehova akhulupirira kolimba;Ndipo ana ace adzakhala ndi pothawirapo.
27. Kuopa Yehova ndiko kasupe wa moyo,Kupatutsa ku misampha ya imfa.
28. Mu unyinji wa anthu muli ulemu wa mfumu;Koma popanda anthu kalonga aonongeka.
29. Wosakwiya msanga apambana kumvetsa;Koma wansontho akuza utsiru.