Miyambi 13:17-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Mthenga wolakwa umagwa m'zoipa;Koma mtumiki wokhulupirika alamitsa.

18. Wokana mwambo adzasauka nanyozedwa;Koma wolabadira cidzudzulo adzalemekezedwa.

19. Cifuniro cikondweretsa moyo citacitidwa;Koma kusiya zoipa kunyansa opusa,

20. Ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru:Koma mnzao wa opusa adzaphwetekedwa.

21. Zoipa zilondola ocimwa;Koma olungama adzalandira mphotho yabwino.

22. Wabwino asiyira zidzukulu zace colowa cabwino;Koma wocimwa angosungira wolungama cuma cace.

23. M'kulima kwa osauka muli zakudya zambiri;Koma zinazo zimaonongeka posowa ciweruzo.

24. Wolekereramwanace osammenya amuda;Koma womkonda amyambize kumlanga.

Miyambi 13