Miyambi 12:25-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

25. Nkhawa iweramitsa mtima wa munthu;Koma mau abwino aukondweretsa.

26. Wolungama atsogolera mnzace;Koma njira ya oipa iwasokeretsa.

27. Wolesi samaocha nyama yace anaigwira;Koma wolungama amalandira cuma copambana ca anthu.

28. M'khwalala la cilungamo muli moyo;M'njira ya mayendedwe ace mulibe imfa.

Miyambi 12