Miyambi 11:28-31 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

28. Wokhulupmra cuma cace adzagwa;Koma olungama adzaphuka ngati tsamba.

29. Wobvuta banja lace adzalowa m'zomsautsa;Wopusa adzatumikira wanzeru.

30. Cipatso ca wolungama ndi mtengo wa moyo;Ndipo wokola mtima ali wanzeru.

31. Taonani, wolungama adzalandira mphotho kunja kuno;Koposa kotani woipa ndi wocimwa?

Miyambi 11