Miyambi 1:9-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Pakuti izi ndi korona wa cisomo pamtu pako,Ndi mkanda pakhosi pako.

10. Mwananga, akakukopa ocimwa usalole.

11. Akanena, Idza nafe, tibisalire mwazi,Tilalire osacimwa opanda cifukwa;

12. Tiwameze ali ndi moyo ngati manda,Ali amphumphu, ngati akutsikira kudzenje;

13. Tidzapeza cuma conse ca mtengo wace,Tidzadzaza nyumba zathu ndi zofunkha;

14. Udzacita nafe maere,Tonse tidzakhala ndi cibeti cimodzi;

15. Mwananga, usayende nao m'njira;Letsa phazi lako ku mayendedwe ao;

16. Pakuti mapazi ao athamangira zoipa,Afulumira kukhetsa mwazi.

17. Pakuti kuchera msampha pamaso pa mbalame ndi cabe;

18. Ndipo awa abisalira mwazi wao wao, alalira miyoyo yao yao.

19. Mayendedwe a yense wopindula cuma monyenga ngotere;Cilanda moyo wa eni ace,

Miyambi 1