4. Ndipo adzaimirira, nadzadyetsa nkhosa zace mu mphamvu ya Yehova, m'ukulu wa dzina la Yehova Mulungu wace; ndipo iwo adzakhalabe; pakuti pamenepo Iye adzakhala wamkuru kufikira malekezero a dziko lapansi.
5. Ndipo ameneyo adzakhala Mtendere; pamene a ku Asuri adzalowa m'dziko lathu, ndi pamene adzaponda m'zinyumba zathu, tidzawaukitsira abusa asanu ndi awiri, ndi akalonga asanu ndi atatu.
6. Ndipo iwo adzatha dziko la Asuri ndi lupanga, ndi dziko la Nimrodi, ndilo polowera pace; ndipo adzatilanditsa kwa a ku Asuri pamene alowa m'dziko lathu, pamene aponda m'kati mwa malire athu.
7. Ndipo otsala a Yakobo adzakhala pakati pa mitundu yambiri ya anthu, ngati mame ocokera kwa Yehova, ngati mvula paudzu, yosacedwera munthu, yosalindira ana a anthu.
8. Ndipo, otsala a Yakobo adzakhala mwa amitundu, pakati pa mitundu yambiri ya anthu, ngati mkango mwa nyama za kuthengo, ngati msona wa mkango mwa magulu a nkhosa; umenewo ukapitako, upondereza, numwetula, ndipo palibe wakupulumutsa.
9. Dzanja lako likwezeke pamwamba pa iwo akuyambana nawe, ndi adani ako onse aonongeke.