1. Uzisonkhana tsopano magulu magulu, mwana wamkazi wa magulu iwe; watimangira misasa, adzapanda woweruza wa Israyeli ndi ndodo patsaya.
2. Koma iwe, Betelehemu Efrata, ndiwe wamng'ono kuti ukhale mwa zikwi za Yuda, mwa iwe mudzanditurukira wina wakudzakhala woweruza m'Israyeli; maturukiro ace ndiwo a kale lomwe, kuyambira nthawi yosayamba.
3. Cifukwa cace Iye adzawapereka kufikira nthawi yoti wobalayo wabala; pamenepo otsala a abale ace adzabwera pamodzi ndi ana a Israyeli,