Mika 1:6-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Cifukwa cace ndidzaika Samariya ngati mulu wa miyala ya m'munda, ngati zooka m'munda wamphesa; ndipo ndidzataya miyala yace m'cigwa, ndi kufukula maziko ace.

7. Ndi mafano ace osema onse adzaphwanyika, ndi mphotho zace zonse zidzatenthedwa ndi moto, ndi mafano ace onse ndidzawapasula; pakuti anazisonkhanitsa pa mphotho ya mkazi waciwerewere, ndipo zidzabwerera ku mphotho ya mkazi waciwerewere.

8. Cifukwa ca ici ndidzacita maliro, ndi kucema, ndidzayenda wolandidwa ndi wamarisece; ndidzalira ngati mimbulu, ndi kubuma ngati nthiwatiwa.

9. Pakuti mabala ace ndi osapola; pakuti afikira ku Yuda; afikira ku cipata ca anthu anga, ku Yerusalemu.

10. Musacifotokoza m'Gati, musalira misozi konse; m'nyumba ya Afira ndinagubuduka m'pfumbi.

11. Pitiratu, wokhala m'Safiri iwe, wamarisece ndi wamanyazi; wokhala m'Zanana sanaturuka; maliro a Betezeli adzakulandani pokhala pace.

12. Pakuti wokhala m'Maroti alindira cokoma, popeza coipa catsika kwa Yehova kumka ku cipata ca Yerusalemu.

Mika 1