14. Ndipo pofika Yesu ku nyumba ya Petro, anaona mpongozi wace ali gone, alikudwala malungo.
15. Ndipo anamkhudza dzanja lace, ndipo malungo anamleka mkaziyo; ndipo anauka, namtumikira Iye.
16. Ndipo pakudza madzulo, anabwera nao kwa Iye anthu ambiri ogwidwa ndi mizimu yoipa; ndipo Iye anaturutsa mizimuyo ndi mau, naciritsa akudwala onse;