Mateyu 8:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo pakutsika pace paphiripo, inamtsata mipingo yambiri ya anthu.

2. Ndipo onani, wakhate anadza namgwadira Iye, nanena, Ambuye ngati mufuna mungathe kundikonza.

3. Ndipo Yesu anatambalitsa dzanja lace, namkhudza iye, nati, Ndifuna; takonzedwa. Ndipo pomwepo khate lace linacoka.

4. Ndipo Yesu ananena naye, Ona, iwe, usauze munthu; koma muka, udzionetse wekha kwa wansembe, nupereke mtulo umene anaulamulira Mose, ukhale mboni kwaiwo.

5. Ndipo m'mene Iye analowa m'Kapernao anadza kwa Iye kenturiyo, nampemba Iye,

6. nati, Ambuye, mnyamata wanga ali gone m'nyumba wodwala manjenje, wozunzidwa koopsa,

7. Ndipo Yesu ananena naye, Ndifika Ine, ndidzamciritsa iye.

Mateyu 8