Mateyu 27:51-53 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

51. Ndipo onani, 10 cinsaru cocinga ca m'Kacisi cinang'ambika pakati, kucokera kumwamba kufikira pansi; ndipo dziko linagwedezeka, ndi miyala inang'ambika;

52. ndi Manda anatseguka, ndi mitembo yambiri ya anthu oyera mtima, akugona kale, inauka;

53. ndipo anaturuka m'manda mwao pambuyo pa kuuka kwace, nalowa m'mzinda woyera, naonekera kwa anthu ambiri.

Mateyu 27